Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 23:6-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Koma mulimbike mtima kwambiri kusunga ndi kucita zonse zolembedwa m'buku la cilamulo ca Mose, osacipambukira kulamanja kapena kulamanzere;

7. osalowa pakati pa amitundu awa otsala mwa inu; kapena kuchula dzina la milungu yao; osalumbiritsa nalo, kapena kuitumikira, kapena kuigwadira;

8. koma muumirire Yehova Mulungu wanu, monga munacita mpaka lero lino.

9. Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikuru ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.

10. Munthu mmodzi wa inu adzapitikitsa anthu cikwi cimodzi; pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye amathirira inu nkhondo monga ananena ndi inu.

11. Potero mudzisamalire ndithu kuti mukonde Yehova Mulungu wanu.

12. Koma, mukadzabwereram'mbuyo pang'ono pokha ndi kuumirira otsala a mitundu awa, ndiwo akutsala pakati pa inu, ndi kukwatitsana nao, ndi kulowana nao, naonso kulowana nanu;

13. dziwani ndithu kuti Yehova Mulungu wanu sadzalandanso dziko la amitundu awa kuwacotsa pamaso panu; koma adzakhala kwa inu deka ndi msampha ndi mkwapulo m'nthiti mwanu, ndi minga m'maso mwanu, mpaka mudzatayika m'dziko lokoma ili anakupatsani Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 23