Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 2:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ali ku Sitimu, anatuma amuna awiri mosadziwika kukazonda, ndi kuti, Mukani, mulipenye dzikolo, ndi ku Yeriko. Ndipo anamuka nalowa m'nyumba ya mkazi wadama, dzina lace Rahabi, nagona momwemo.

2. Ndipo wina anaiuza mfumu ya Yeriko, kuti, Taonani, usiku uno alowa muno amuna a ana a Israyeli, kulizonda dziko.

3. Ndipo mfumu ya Yeriko inatuma wina kwa Rahabi, ndi kuti, Turutsa amunawo anafika kwanu, amene analowa m'nyumba mwako; popeza anadzera kulizonda dziko lonse.

4. Koma mkaziyo anatenga amuna awiriwo, nawabisa; natero, Inde, amunawo anandifikira; koma sindinadziwa uko afuma;

5. ndipo m'mene akadati atseke pacipata, kutada, anaturuka amunawo; uko anamuka amunawo osakudziwa ine; muwalondole msanga, pakuti mudzawapeza.

6. Koma adawakweretsa patsindwi, nawabisa ndi mitengo yanthamza yoyanika patsindwi.

7. Ndipo amunawo anawalondola pa njira ya ku Yordano yomka kudooko; ndipo ataturuka akuwalondola, anatseka pacipata.

8. Koma asanagone iwo, anawakwerera patsindwi iye,

9. nati kwa amunawo, Ndidziwa kuti Yehova wakupatsani dzikoli, ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m'dziko onse asungunuka pamaso panu.

10. Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m'Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudaruruka m'Aigupto; ndi cija munacitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya la Yordano, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawaononga konse.

11. Ndipo titamva ici mitima yathu inasungunuka; anahbenso mtima ndi mmodzi yense, cifukwa ca inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m'mwamba umo, ndi pa dziko lapansi.

12. Ndipo tsopano, mundilumbiriretu kwa Yehova, popeza ndakucitirani cifundo, kuti inunso mudzacitira cifundo a m'nyumba ya atate wanga ndi kundipatsa cizindikilo coona,

13. kuti mudzawasunga ndi moyo atate wanga ndi mai wanga, ndi alongo anga ndi abale anga, ndi zonse ali nazo, ndi kupulumutsa miyoyo yathu kuimfa.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 2