15. Ndipo Yoswa ananena nao, Ngati muli anthu aunyinji, kwerani kuli mitengoko, ndi kudziswera minda m'dziko la Aperizi ndi la Arefai; akakuceperani malo ku phiri la Efraimu.
16. Ndipo ana a Yosefe anati, Kuphiriko sikudzatifikira; ndipo Akananionse akukhala m'dziko la cigwa ali nao magareta acitsulo, iwo akukhala m'Bete-Seani, ndi midzi yace ndi iwo omwe akukhala m'cigwa ca Yezereli.
17. Ndipo Yoswa ananena kwa iwo a m'nyumba ya Yosefe, kwa Efraimu ndi Manase, ndi kuti, Inu ndinu anthu aunyinji, muli nayo mphamvu yaikuru; simudzakhala nalo gawo limodzi lokha;
18. koma kuphiriko kudzakhala kwanu pakuti pangakhale mpa mitengo, mudzisweretu minda, ndi maturukiro ace adzakhala anu; pakuti mudzaingitsa Akanani angakhale ali nao magareta acitsulo, angakhale ali amphamvu.