Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 15:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo malire anazungulira kuyambira ku Baala kumka kumadzulo, ku phiri la Seiri, napitirira kumbali kwa phiri la Yearimu kumpoto, ndilo Kesaloni, natsikira ku Beti-semesi, napitirira ku Timina;

11. naturuka malire kumka ku mbali ya Ekroni kumpoto; ndipo analemba malire kumka ku Sikeroni, napitirira ku phiri la Baala, naturuka ku Yabindi; ndipo maturukiro a malire anali kunyanja.

12. Ndi malire a kumadzulo anali ku Nyanja Yaikuru ndiwo malire ace. Awa ndi malire a ana a Yuda pozungulira monga mwa mabanja ao.

13. Koma Yoswa anampatsa Kalebe mwana wa Yefune gawo mwa ana a Yuda, monga Yehova adamlamulira, ndiwo mudzi wa Ariba, ndiye atate wa Anaki, ndiwo Hebroni.

14. Ndipo Kalebe anaingitsako ana amuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.

15. Nakwera komweko kumka kwa nzika za Dibiri; koma kale dzina la Dibiri ndilo Kiriyati-Seferi.

16. Ndipo Kalebe anati, iye amene akantha Kiriyati-Seferi, naulanda, yemweyo ndidzampatsa Akisa mwana wanga akhale mkazi wace.

17. Ndipo Otiniyeli mwana wa Kenazi, mbale wace wa Kalebe, anaulanda; ndipo anampatsa Akisa mwana wace akhale mkazi wace.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 15