1. Ndipo gawo la pfuko la ana a Yuda monga mwa mabanja ao linafikira malire a Edomu, ku cipululu ca Zini kumwera, ku malekezero a kumwera.
2. Ndi malire ao a kumwera, anayambira ku malekezero a Nyanja ya Mcere, ku nyondo yoloza kumwera;
3. naturuka kumwela kwa cikweza ca Akarabi, napitirira ku Zini, nakwera kumwera kwa Kadesi-Barinea, napitirira ku Hezironi, nakwera ku Adara, nazungulira ku Karika;
4. napitirira ku Azimoni, naturuka ku mtsinje wa Aigupto; ndi malekezero a malirewa anali ku Nyanja Yaikuru; awa ndi malire anu a kumwera.
5. Ndi malire a kum'mawa ndiwo Nyanja ya Mcere, mpaka mathiriro ace a Yordano. Ndi malire a kumpoto anayambira nyondo ya nyanja ku mathiriro a Yordano;
6. nakwera malire kumka ku Beti-hogila, napitirira kumpoto kwa Beti-araba; nakwera malire kumka ku mwala wa Bohani mwana wa Rubeni;