Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 14:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo awa ndi maiko ana a Israyeli anawalanda m'dziko la Kanani, amene Eleazare wansembe, ndi Yoswa mwana wa Nuni, ndi akulu a nyumba za atate a mapfuko a ana a Israyeli, anawagawira.

2. Kulandira kwao kunacitika ndi kulota maere, monga Yehova adalamulira mwa dzanja la Mose, kunena za mapfuko asanu ndi anai ndi pfuko logawika pakati.

3. Pakuti Mose adapatsa mapfuko awiri, ndi pfuko logawika pakati, colowa tsidya ito la Yordano; koma sanapatsa Alevi colowa pakati pao,

4. Pakuti ana a Yosefe ndiwo mapfuko awiri, Manase ndi Efraimu; ndipo sanawagawira Alevi kanthu m'dziko, koma midzi yokhalamo ndi dziko lozungulirako likhale la zoweta zao ndi cuma cao.

5. Monga Yehova analamulira Mose, momwemo ana a Israyeli anacita, nagawana dziko.

6. Pamenepo ana a Yuda anadza kwa Yoswa ku Giligala; ndi Kalebe mwana wa Yefune Mkenizi ananena naye, Mudziwa cimene Yehova adanena kwa Mose munthu wa Mulungu za ine ndi za inu m'KadesiBarinea.

7. Ndinali ine wa zaka makumi anai muja Mose mtumiki wa Yehova anandituma kucokera ku Kadesi-Barinea, kukazonda dziko; ndipo ndinambwezera mau, monga momwe anakhala mumtima mwanga.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 14