Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 13:7-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo tsopano uwagawire mapfuko asanu ndi anai, ndi pfuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale colowa cao.

8. Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira colowa cao, cimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordano kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

9. kuyambira pa Aroeri, wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uti pakati pa cigwa, ndi cidikha conse ca Medeba mpaka ku Diboni;

10. ndi midzi yonse ya Sihoni mfumu ya Aamori, wakucita ufumu m'Hesiboni, mpaka malire a ana a Amoni;

11. ndi Gileadi, ndi malire a Agesuri, ndi Amaakati, ndi phiri lonse la Herimoni, ndi Basana ionse mpaka ku Saleka;

12. ufumu wonse wa Ogi m'Basana, wakucita ufumu m'Asitarotu, ndi m'Edrei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefai); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.

13. Koma ana a Israyeli sanainga Agesuri kapena Amaakati; koma Gesuri, ndi Maakati amakhala pakati pa Israyeli, mpaka lero lino.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 13