Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 13:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Yoswa anakalamba, wa zaka zambiri; ndipo Yehova ananena naye, Wakalamba, wa zaka zambiri, ndipo latsala dziko lalikurukuru, alilandire colowa cao,

2. Dziko lotsala ndilo: malire onse a Afilisti, ndi Agesuri onse,

3. kuyambira Sihoro wokhala cakuno ca Aigupto mpaka malire a Ekironu kumpoto, loyesedwa la Akanani; akalonga asanu a Afilisti, a ku Gaza, ndi a ku Asidodi, a ku Asekelo, a ku Giti, ndi a ku Ekiro, ndi Ahivi;

4. kumwela dziko lonse la Akanani, ndi Meara ndiwo wa Asidoni, mpaka ku Afeka, mpaka ku malire a Aaroori;

5. ndi dziko la Agebili, ndi Lebano lonse kum'mawa, kuyambira Baala-gadi pa tsinde la phiri la Herimoni, mpaka polowera pace pa Hamati;

6. nzika zonse za kumapiri kuyambira Lebano, mpaka Misirepotumaimu, Asidoni onse; ndidzawainga pamaso pa ana a Israyeli, koma limeneli uwagawire Aisrayeli, likhale colowa cao, monga ndinakulamulira.

7. Ndipo tsopano uwagawire mapfuko asanu ndi anai, ndi pfuko la Manase logawika pakati, dziko ili likhale colowa cao.

8. Pamodzi ndi iye Arubeni ndi Agadi analandira colowa cao, cimene Mose adawapatsa tsidya ilo la Yordano kum'mawa, monga Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa;

9. kuyambira pa Aroeri, wokhala m'mphepete mwa cigwa ca Arinoni, ndi mudzi uti pakati pa cigwa, ndi cidikha conse ca Medeba mpaka ku Diboni;

Werengani mutu wathunthu Yoswa 13