6. Mose mtumiki wa Yehova ndi ana a Israyeli anawakantha; ndi Mose mtumiki wa Yehova analipereka kwa Arubeni, ndi Agadi ndi pfuko la Manase logawika pakati, likhale colowacao.
7. Ndipo awa ndi mafumu a dzikolo amene Yoswa ndi ana a Israyeli anawakantha tsidya lija la Yordano kumadzulo, kuyambira Baala-gadi m'cigwa ca Lebano mpaka phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri; ndipo Yoswa analipereka kwa mapfuko a Israyeli, likhale lao lao, monga mwa magawo ao;
8. kumapiri ndi kucigwa, ndi kucidikha, ndi kumatsikiro, ndi kucipululu, ndi kumwela: Ahiti, Aamori, ndi Akanani, Aperizi, Ahivi ndi Ayebusi:
9. mfumu ya ku Yeriko, imodzi; mfumu ya ku Ai, ndiwo m'mbali mwa Beteli, imodzi;
10. mfumu ya ku Yerusalemu, imodzi; mfumu ya ku Hebroni, imodzi; mfumu ya ku Yarimutu, imodzi;
11. mfumu ya ku Lakisi, imodzi;
12. mfumu ya ku Egiloni, imodzi; mfumu ya ku Gezere, imodzi;
13. mfumu ya ku Dibiri, imodzi; mfumu ya ku Gederi, imodzi;
14. mfumu ya ku Horima, imodzi; mfumu ya ku Haradi, imodzi;
15. mfumu ya ku Libina, imodzi; mfumu ya ku Adulamu, imodzi;
16. mfumu ya ku Makeda, imodzi; mfumu ya ku Beteli, imodzi;
17. mfumu ya ku Tapuwa, imodzi; mfumu ya ku Heferi, imodzi;
18. mfumu ya ku Afeki, imodzi; mfumu ya ku Lasaroni, imodzi;
19. mfumu ya ku Madoni, imodzi; mfumu ya ku Hazori, imodzi;
20. mfumu ya ku Simironi-meroni, imodzi; mfumu ya ku Akasafu, imodzi;