Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 11:17-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. kuyambira phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri, mpaka Baala-gadi m'cigwa ca Lebano patsinde pa phiri la Herimoni; nagwira mafwnu ao onse, nawakantha, nawapha.

18. Yoswa anathira nkhondo mafwnu awa onse nthawi yaikuru.

19. Palibe mudzi wakupangana mtendere ndi ana a Israyeli, koma Ahivi okhala m'Gibeoni; anaigwira yonse ndi nkhondo.

20. Pakuti cidadzera kwa Yehova kulimbitsa mitima yao kuti athirane nao Aisrayeli nkhondo kuti iye awaononge konse, kuti asawacitire cifundo koma awaononge, monga Yehova adalamulira Mose.

21. Ndipo Yoswa anadza nthawi yomweyo, napasula Aanaki kuwacotsa kumapiri, ku Hebroni, ku Dibiri, ku Anabi, ndi ku mapiri onse a Yuda, ndi ku mapiri onse a Israyeli; Yoswa anawaononga konse, ndi midzi yao yomwe.

22. Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israyeli; koma m'Gaza, ndi m'Gati ndi m'Asidodo anatsalamo ena.

23. Motero Yoswa analanda dziko lonse monga mwa zonse Yehova adazinena kwa Mose; ndipo Yoswa analipereka kwa Israyeli, likhale lao lao, pfuko liri lonse gawo lace. Ndipo dziko linapumula nkhondo.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 11