Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 11:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Ndipo Yoswa anabwerera m'mbuyo nthawi imeneyi nalanda Hazori nakantha mfumu yace ndi lupanga; pakuti kale Hazori unali waukuru wa maufumu aja onse.

11. Ndipo anakantha amoyo onse anali m'mwemo, ndi lupanga lakuthwa, ndi kuwaononga konse, osasiyapo ndi mmodzi yense wakupuma mpweya; ndipo anatentha Hazori ndi moto.

12. Ndipo Yoswa analanda midzi yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.

13. Koma midzi yonse yomangidwa pa zitunda zao Israyeli sanaitentha, koma wa Hazori wokha; wnenewu Yoswa anautentha.

14. Ndi zofunkha zonse za midzi iyi ndi ng'ombe ana a Israyeli anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.

15. Monga Yehova adalamulira Mose mtumiki wace, momwemo Mose analamulira Yoswa; momwemonso anacita Yoswa; sanacotsapo mau amodzi pa zonse Yehova adalamulira Mose.

16. Motero Yoswa analanda dziko lonselo, la kumapiri, ndi la kumwera, ndi dziko lonse la Goseni, ndi dziko la kucidikha, ndi la kucigwa; ndi la kwnapiri la Israyeli, ndi la ku cidikha cace;

17. kuyambira phiri la Halaki lokwera kumka ku Seiri, mpaka Baala-gadi m'cigwa ca Lebano patsinde pa phiri la Herimoni; nagwira mafwnu ao onse, nawakantha, nawapha.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 11