Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 10:37-43 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

37. naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anacitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.

38. Pamenepo Yoswa, ndi Aisrayeli onse naye, anabwerera kudza ku Dibiri, nauthira nkhondo,

39. naulanda, ndi mfumu yace ndi midzi yace yonse; naikantha ndi lupanga lakuthwa, naononga konse amoyo onse anali m'mwemo; sanasiya ndi mmodzi yense; monga anacitira Hebroni momwemo anacitira Dibiri ndi mfumu yace, monganso anacitira Libina ndi mfumu yace.

40. Motero Yoswa anakantha dziko lonse, la kumapiri, la kumwela, la kucidikha, la kuzigwa, ndi mafumu ao onse; sanasiyapo ndi mmodzi yense; koma anaononga psiti zonse zampweya, monga Yehova Mulungu wa Israyeli adalamulira.

41. Ndipo Yoswa anawakantha kuyambira Kadesi-Barinea mpaka ku Gaza, ndi dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibeoni.

42. Ndipo Yoswa anagwira mafwnu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; cifukwa Yehova Mulungu wa Israyeli anathirira Israyeli nkhondo.

43. Pamenepo Yoswa ndi Aisrayeli onse naye, anabwerera kucigono ku Giligala.

Werengani mutu wathunthu Yoswa 10