Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yoswa 1:4-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. Kuyambira cipululu, ndi Lebano uyu, kufikira mtsinje waukulu mtsinje wa Firate, dziko lonse la Ahiti, ndi kufikira nyanja yaikuru ku malowero a dzuwa, ndiwo malire anu.

5. Palibe munthu adzatha kuima pamaso pako masiku onse a moyo wako; monga ndinakhala ndi Mose momwemo ndidzakhala ndi iwe; sindidzakusowa, sindidzakusiya.

6. Khala wamphamvu, nulimbike mtima, pakuti udzagawira anthu awa dzikoli likhale colowa cao, ndilo limene ndinalumbirira makolo ao kuwapatsa.

7. Komatu khala wamphamvu, nulimbike mtima kwambiri, kuti usamalire kucita monga mwa cilamulo conse anakulamuliraco Mose mtumiki wanga; usacipambukire ku dzanja lamanja kapena kulamanzere, kuti ukacite mwanzeru kuli konse umukako.

8. Buku ili la cilamulo lisacoke pakamwa pako; koma ulingiriremo usana ndi usiku, kuti usamalire kucita monga mwa zonse zolembedwamo; popeza ukatero udzakometsa njira yako, nudzacita mwanzeru.

9. Kodi sindinakulamulira iwe? Khala wamphamvu, nulimbike mtima, usaope, kapena kutenga nkhawa, pakuti Yehova Mulungu wako ali ndi iwe kuli konse umukako.

10. Pamenepo Yoswa analamulira akapitao a anthu, ndi kuti,

Werengani mutu wathunthu Yoswa 1