Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yobu 14:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Munthu wobadwa ndi mkaziNgwa masiku owerengeka, nakhuta mabvuto,

2. Aturuka ngati duwa, nafota;Athawa ngati mthunzi, osakhalitsa.

3. Ndipo kodi mumtsegulira maso anu wotereyo,Ndi kunditenga kunena nane mlandu Inu?

4. Adzaturutsa coyera m'cinthu codetsa ndani? nnena mmodzi yense.

Werengani mutu wathunthu Yobu 14