Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 9:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma kumene kunali nsautso sikudzakhala kuziya. Poyamba paja Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni, ndi dziko la Naftali, koma potsiriza pace Iye analicitira ulemu, pa khwalala la kunyanja, patsidya pa Yordano, Galileya wa amitundu.

2. Anthu amene anayenda mumdima, aona kuwala kwakukuru; iwo amene anakhala m'dziko la mthunzi wa imfa, kuwala kwaturukira kwa iwo.

3. Inu mwacurukitsa mtundu, inu mwaenjezera kukondwa kwao; iwo akondwa pamaso panu monga akondwera m'masika, monga anthu akondwa pogawana zofunkha.

4. Pakuti gori la katundu wace, ndi mkunkhu wa paphewa pace, ndodo ya womsautsa, inu mwazityola monga tsiku la Midyani.

5. Pakuti zida zonse za mwamuna wobvala zida za nkhondo m'phokosomo, ndi zobvala zobvimvinika m'mwazi, zidzakhala zonyeka ngati nkhuni.

6. Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lace, ndipo adzamucha dzina lace Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 9