Iwe sudzachedwanso Wosiyidwa; dziko lako silidzachedwanso Bwinja; koma iwe udzachedwa Hefiziba ndi dziko lako Beula; pakuti Yehova akondwera mwa iwe, ndipo dziko lako lidzakwatiwa.