Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 60:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwake kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakuturukira.

2. Pakuti taona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu; koma Yehova adzakuturukira, ndi ulemerero wace udzaoneka pa iwe.

3. Ndipo amitundu adzafika kwa kuunika kwako, ndi mafumu kwa kuyera kwa kuturuka kwake,

4. Tukula maso ako uunguze-unguze ndi kuona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzacokera kutari, ndi ana ako akazi adzaleredwa pambali.

5. Pamenepo udzaona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthunthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, cuma ca amitundu cidzafika kwa iwe.

6. Gulu la ngamila lidzakukuta, ngamila zazing'ono za Midyani ndi Efa; iwo onsewo adzacokera ku Seba adzabwera nazo golidi ndi zonunkhira; ndipo adzalalikira matamando a Yehova.

7. Zoweta za Kedara zidzasonkhana kwa iwe, nkhosa zamphongo za Nebaioti zidzakutumikira; izo zidzafika ndi kulandiridwa pa guwa langa la nsembe; ndipo ndidzakometsa nyumba ya ulemerero wanga.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 60