Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 58:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Koma iwo andifuna Ine tsiku ndi tsiku, ndi kukondwera kudziwa njira zanga; monga mtundu wa anthu ocita cilungamo, osasiya cilangizo ca Mulungu wao, iwo andipempha Ine zilangizo zolungama, nakondwerera kuyandikira kwa Mulungu.

3. Amati, Bwanji ife tasala kudya, ndipo Inu simuona? ndi bwanji ife tabvutitsa moyo wathu, ndipo Inu simusamalira? Taonani, tsiku la kusala kudya kwanu inu mupeza kukondwerera kwanu, ndi kutsendereza anchito anu onse.

4. Taonani, inu musala kudya kuti mukangane ndi kutsutsana ndi kukantha ndi nkhonya yoipa; inu simusala kudya tsiku lalero kuti mumveketse mau anu kumwamba.

5. Kodi kusala kudya koteroko ndiko ndinakusankha? tsiku lakubvutitsa munthu moyo wace? Kodi ndiko kuweramitsa mutu wace monga bango, ndi kuyala ciguduli ndi phulusa pansi pace? Kodi uyesa kumeneko kusala kudya, ndi tsiku lobvomerezeka kwa Yehova?

6. Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga gori, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti mutyole magori onse?

7. Kodi si ndiko kupatsa cakudya cako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? pakuona wamalisece kuti umbveke, ndi kuti usadzibisire wekha a cibale cako?

8. Pomwepo kuunika kwako kudzawalitsa monga m'mawa, ndi kucira kwako kudzaonekera msanga msanga; ndipo cilungamo cako cidzakutsogolera; ulemerero wa Yehova udzakhala wocinjiriza pambuyo pako.

9. Pamenepo udzaitana, ndipo Yehova adzayankha; udzapfuula ndipo Iye adzati, Ndine pano. Ngati ucotsa pakati pa iwe gori, kukodolana moipa, ndi kulankhula moipa,

Werengani mutu wathunthu Yesaya 58