5. Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?
6. Pakuti pa miyala yosalala ya m'cigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?
7. Pamwamba pa phiri lalitaritari unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.
8. Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa cikumbutso cako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.