Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 57:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Wolungama atayika, ndipo palibe munthu wosamalirapo; ndipo anthu acifundo atengedwa, palibe wolingalira kuti wolungama acotsedwa pa coipa cirinkudza.

2. Iye alowa mumtendere, iwo apuma pa mphasa zao, yense woyenda moongoka.

3. Koma sendererani kuno cifupi, inu ana amuna a watsenga, mbeu yacigololo ndi yadama.

4. Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumturutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?

5. Inu amene muutsa zilakolako zanu pakati pa mathundu, patsinde pa mitengo yonse ya gudugudu, amene mupha ana m'zigwa pansi pa mapanga a matanthwe?

6. Pakuti pa miyala yosalala ya m'cigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?

7. Pamwamba pa phiri lalitaritari unayala mphasa yako; kumenekonso wakwera kukapereka nsembe.

8. Ndi kumbuyo kwa zitseko ndi mphuthu waimiritsa cikumbutso cako, pakuti wadzionetsa wekha kwa wina, wosati kwa Ine; ndipo wakwerako, wakuza mphasa yako, ndi kupangana nao pangano; unakonda mphasa yao kumene unaiona.

9. Ndipo unanka kwa mfumu, utadzola mafuta ndi kucurukitsa zonunkhira zako; ndipo unatumiza atumwi ako kutari; ndipo wadzicepetsa wekha kufikira kunsi ku manda.

10. Unatopa ndi njira yako yaitari; koma sunanene, Palibe ciyembekezo; iwe wapeza moyo wa dzanja lako; cifukwa cace sunalefuka.

11. Ndipo ndi yani amene wamuopa ndi kucita naye mantha, kuti wanama, osandikumbukira Ine, kapena kundisamalira? Kodi Ine sindinakhala cete nthawi yambiri, ndipo iwe sunandiopa Ine konse?

Werengani mutu wathunthu Yesaya 57