Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 55:2-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Bwanji inu mulikutayira ndarama cinthu cosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye cimene ciri cabwino, moyo wanu nubondwere ndi zonona.

3. Cherani Lhutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu cipangano cosatha, ndico zifundo zoona za Davide.

4. Taonani, ndampereka iye akhale mboni ya anthu, wotsogolera ndi wolamulira anthu.

5. Taona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziwa, ndi mtundu umene sunakudziwa udzakuthamangira, cifukwa ca Yehova Mulungu wako, ndi cifukwa ca Woyera wa Israyeli; pakuti Iye wakukometsa.

6. Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;

7. woipa asiye njira yace, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ace, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamcitira cifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

8. Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu siziri njira zanga, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 55