Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 54:8-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. M'kukwiya kwa kusefukira ndinakubisira nkhope yanga kamphindi; koma ndi kukoma mtima kwa cikhalire ndidzakucitira cifundo, ati Yehova Mombolo wako.

9. Pakuti kumeneku kuli kwa Ine monga madzi a Nowa; pakuti monga ndinalumbira kuti madzi a Nowa sadzamizanso pa dziko lapansi, momwemo ndinalumbira kuti sindidzakukwiyira iwe, pena kukudzudzula.

10. Pakuti mapiri adzacoka, ndi zitunda zidzasunthika; koma kukoma mtima kwanga sikudzakucokera iwe, kapena kusunthika cipangano canga ca mtendere, ati Yehova amene wakucitira iwe cifundo.

11. Iwe wosautsidwa, wobelukabeluka ndi namondwe, wosatonthola mtima, taona, ndidzakhazika miyala yako m'maanga-maanga abwino, ndi kukhazika maziko ako ndi masafiro.

12. Ndipo ndidzamanga mazenera ako ndi miyala yofiira, ndi zipata zako ndi bareketi, ndi malire ako onse ndi miyala yokondweretsa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 54