Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 53:5-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Koma Iye analasidwa cifukwa ca zolakwa zathu, natundudzidwa cifukwa ca mphulupulu zathu; cilango cotitengera ife mtendere cinamgwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yace ife taciritsidwa.

6. Tonse tasocera ngati nkhosa; tonse tayenda yense m'njira ya mwini yekha; ndipo Yehova anaika pa Iye mphulupulu ya ife tonse.

7. Iye anatsenderezedwa koma anadzicepetsa yekha osatsegula pakamwa pace; ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa, ndi ngati mwana wa nkhosa amene ali du pamaso pa omsenga, motero sanatsegula pakamwa pace.

8. Anacotsedwa ku cipsinjo ndi ciweruziro; ndipo ndani adzafotokoza nthawi ya moyo wace? pakuti walikhidwa kunja kuno; cifukwa ca kulakwa kwa anthu anga Iye anakhomedwa.

9. Ndipo anaika manda ace pamodzi ndi oipa, ndi pamodzi ndi olemera mu imfa yace, ngakhale Iye sanacita ciwawa, ndipo m'kamwa mwace munalibe cinyengo.

10. Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wace ukapereka nsembe yoparamula, Iye adzaona mbeu yace, adzatanimphitsa masiku ace; ndipo comkondweretsa Yehova cidzakula m'manja mwace.

11. Iye adzaona zotsatira mabvuto a moyo wace, nadzakhuta nazo; ndi nzeru zace mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri, nadzanyamula mphulupulu zao.

12. Cifukwa cace ndidzamgawira gawo ndi akuru; ndipo adzagawana ndi amphamvu zofunkha; pakuti Iye anathira moyo wace kuimfa; ndipo anawerengedwa pamodzi ndi olakwa; koma ananyamula macimo a ambiri, napembedzera olakwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 53