5. Cilungamo canga ciripafupi, cipulumutso canga camuka; ndipo mikono yanga idzaweruza anthu; zisumbu zidzandilindira, ndipo adzakhulupirira mkono wanga.
6. Tukulani maso anu kumwamba, ndipo muyang'ane pansi pa dziko; pakuti kumwamba kudzacoka ngati utsi, ndi dziko lidzatha ngati copfunda, ndipo iwo amene akhala m'menemo adzafa cimodzimodzi; koma cipulumutso canga cidzakhala ku nthawi lonse, ndi cilungamo canga sicidzacotsedwa.
7. Mverani Ine, inu amene mudziwa cilungamo, anthu amene mumtima mwao muli lamulo langa; musaope citonzo ca anthu, ngakhale kuopsedwa ndi kutukwana kwao.
8. Pakuti njenjete idzawadya ngati copfunda, ndi mbozi zidzawadya ngati ubweya; koma cilungamo canga cidzakhala ku nthawi zonse, ndi cipulumutso canga ku mibadwo yonse.
9. Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjiri zipinjiri, amene unapyoza cinjoka cija?
10. Kodi si ndiwe amene unaumitsa nyanja, madzi akuya kwambiri; amene anasandutsa nyanja zikhale njira ya kupitapo oomboledwa?
11. Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika ku Ziyoni; ndi nyimbo ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; adzakhala m'kusangalala ndi kukondwa, ndipo cisoni ndi kuusa moyo kudzacoka.
12. Ine, Inedi, ndine amene nditonthoza mtima wako; kodi iwe ndani, kuti uopa munthu amene adzafa, ndi mwana wa munthu amene adzakhala ngati udzu;