Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 5:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndiyimbire wokondedwa wanga nyimbo ya wokondedwa wanga ya munda wace wamphesa, Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa m'citunda ca zipatso zambiri;

2. ndipo iye anakumba mcerenje kuzungulira kwete, natolatola miyala pamenepo naokapo mpesa wosankhika, namangapo pakati pace nsanja, nasema mopondera mphesa, nayembekeza kuti udzabala mphesa, koma unangobala mphesa zosadya.

3. Ndipo tsopano, inu okhala m'Yerusalemu, ndi anthu a Yuda, weruzanitu mlandu wa ine ndi munda wanga wamphesa.

4. Ndikanacitanso ciani ndi munda wanga wamphesa, cimene sindinacite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?

5. Ndipo tsopano ndidzakuuzani cimene nditi ndicite ndi munda wanga wamphesa; ndidzacotsapo chinga lace, ndipo zidzadyedwa; ndidzagumula linga lace, ndipo zidzapondedwa pansi;

6. ndipo ndidzaupasula; sudzadzomboleredwa kapena kulimidwa; koma padzamera lunguzi ndi minga; ndidzalamuliranso mitambo kuti isabvumbwepo mvula.

7. Cifukwa kuti munda wamphesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israyeli, ndi anthu a Yuda, mtengo wace womkondweretsa; Iye anayembekeza ciweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza cilungamo, koma onani kupfuula.

8. Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati pa dziko!

9. M'makutu anga, ati Yehova wa makamu, Zoonadi nyumba zambiri zidzakhala bwinja, ngakhale zazikuru ndi zokoma zopanda wokhalamo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 5