Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 48:1-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Imvani inu ici, banja la Yakobo, amene muchedwa ndi dzina la Israyeli, amene munaturuka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kuchula dzina la Mulungu wa Israyeli, koma si m'zoona, pena m'cilungamo.

2. Pakuti adziyesa okha a mudzi wopatulika, ndi kudzikhazikitsa iwo okha pa Mulungu wa Israyeli; dzina lace ndi Yehova wa makamu.

3. Ndanena zinthu zoyamba kuyambira kale; inde, izo zinaturuka m'kamwa mwanga, ndipo ndinazisonyeza; mwadzidzidzi ndinazicita izo, ndipo zinaoneka.

4. Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako liri mtsempha wacitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;

5. cifukwa cace ndinakudziwitsa ici kuyambira kale; cisanaoneke ndinakusonyeza ico, kuti iwe unganene, Fano langa lacita izo, ndi cifanizito canga cosema, ndi cifaniziro canga coyenga zinazilamulira.

6. Iwe wacimva taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzacinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kucokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.

7. Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.

8. Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde, kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wacita mwaciwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa cibadwire.

9. Cifukwa ca dzina langa ndidzacedwetsa mkwiyo wanga, ndi cifukwa ca kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakucotse.

10. Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.

11. Cifukwa ca Ine ndekha, cifukwa ca Ine ndekha ndidzacita ici, pakuti dzina langa lidetsedwerenji? ndi ulemerero wanga sindidzaupereka kwa wina.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 48