Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 47:2-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Tenga mipero, nupere ufa; cotsa cophimba cako, bvula copfunda, kwinda m'mwendo, oloka mitsinje.

3. Marisece ako adzakhala osapfundidwa, inde, manyazi ako adzaoneka; ndidzacita kubwezera, osasamalira munthu.

4. Mombolo wathu, Yehova wa makamu ndi dzina lace, Woyera wa Israyeli.

5. Khala iwe cete, lowa mumdima, mwana wamkazi wa Akasidi; pakuti sudzachedwanso mkazi wa maufumu.

6. Ndinakwiyira anthu anga, ndinaipitsa colowa canga, ndi kuwapereka m'manja ako; koma iwe sunawaonetsera cifundo; wasenzetsa okalamba goli lako lolemera ndithu.

7. Ndipo unati, Ndidzakhala mkazi wa mfumu wa nthawi zonse; ndipo sunasamalira izi mumtima mwako, kapena kukumbukira comarizira cace.

8. Cifukwa cace tsono, imva ici, iwe wotsata zokondweretsa, amene umakhala mosatekeseka, amene umati mumtima mwako, Ine ndine, ndipo popanda ine palibenso wina; sindidzakhala monga mkazi wamasiye, kapena kudziwa kumwalira kwa ana;

9. koma izi ziwiri zidzakugwera mwadzidzidzi, tsiku limodzi kumwalira kwa ana ndi umasiye zidzakugwera; mokwanira monse, pakati pa unyinji wa matsenga ako, ndi pakati pa maphenda ako ambirimbiri.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 47