Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 43:21-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.

22. Komabe iwe sunandiitane Ine, Yakobo; koma iwe walema ndi Ine, Israyeli.

23. Iwe sunanditengere Ine zoweta zazing'ono za nsembe zopsereza zako; kapena kundilemekeza ndi nsembe zako. Sindinakutumikiritsa ndi nsembe zaufa, kapena kukutopetsa ndi zonunkhira.

24. Iwe sunandigulire Ine nzimbe ndi ndarama, pena kundikhutitsa ndi mafuta a nsembe zako. Koma iwe wanditumikiritsa ndi macimo ako, wanditopetsa ndi mphulupulu zako.

25. Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, cifukwa ca Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira macimo ako.

26. Undikumbutse Ine; tiyeni, tinenane pamodzi; fotokoza mlandu wako, kuti ukalungamitsidwe.

27. Atate wako woyamba anacimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine.

28. Cifukwa cace ndidzaipitsa akuru a kacisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israyeli akhale citonzo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 43