Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 43:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma tsopano atero Yehova, amene anakulenga iwe Yakobo, ndi Iye amene anakupanga iwe Israyeli, Usaope, cifukwa ndakuombola iwe, ndakuchula dzina lako, iwe uli wanga.

2. Pamene udulitsa pamadzi ndiri pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsya; ngakhale lawi silidzakutentha.

3. Cifukwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wako, Woyera wa Israyeli, Mpulumutsi wako; ndapatsa Aigupto dombolo lako, Etiopia ndi Seba m'malo mwako.

4. Pokhala iwe wa mtengo wapatari pamaso panga, ndi wolemekezeka, ndipo ndakukonda iwe; Ine ndidzakuombola ndi anthu, ndi kupereka anthu m'malo mwa moyo wako.

5. Usaope; pakuti Ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbeu zako kucokera kum'mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kucokera kumadzulo.

6. Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kumwera, Usaletse; bwera nao ana anga amuna kucokera kutari, ndi ana anga akazi kucokera ku malekezero a dziko lapansi;

7. yense wochedwa dzina langa, amene ndinamlenga cifukwa ca ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.

8. Turutsani anthu akhungu, amene ali ndi maso, ndi agonthi, amene ali ndi makutu.

9. Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.

10. Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 43