Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.