Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 41:7-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Cotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golidi, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi nthobvu, Kuti kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8. Koma iwe, Israyeli, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

9. iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kucokera m'ngondya zace, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;

10. usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.

11. Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 41