Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 41:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Zisumbu zinaona niziopa; malekezero a dziko lapansi ananthunthumira; anayandikira, nafika.

6. Iwo anathangata yense mnansi wace, ndi yense anati kwa mbale wace, Khala wolimba mtima.

7. Cotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golidi, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi nthobvu, Kuti kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.

8. Koma iwe, Israyeli, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;

9. iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kucokera m'ngondya zace, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;

10. usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.

11. Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 41