Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 40:6-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Mau a wina ati, Pfuula. Ndipo ndinati, Kodi ndipfuule ciani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;

7. udzu unyala, duwa lifota; cifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.

8. Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zacikhalire.

9. Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitari; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena ku midzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!

10. Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wace udzalamulira; taonani, mphoto yace iri ndi Iye, ndipo cobwezera cace ciri patsogolo pa Iye.

11. Iye adzadyetsa zoweta zace ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pacapa pace, nadzawatengera pa cifuwa cace, ndipo adzatsogolera bwino bwino zimene ziyamwitsa.

12. Ndani wayesa madzi m'dzanja lace, nayesa thambo ndi cikhato, ndi kudzaza pfumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?

13. Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lace, ndi kumphunzitsa Iye?

14. Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya ciweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?

15. Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati pfumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 40