Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 40:2-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

2. Munene inu zotonthoza mtima kwa Yerusalemu, nimupfuulire kwa iye, kuti nkhondo yace yatha, kuti kuipa kwace kwakhululukidwa; kuti iye walandira mowirikiza m'dzanja la Yehova, cifukwa ca macimo ace onse.

3. Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti se khwalala la Mulungu wathu.

4. Cigwa ciri conse cidzadzazidwa, ndipo phiri liri lonse ndi citunda ciri conse zidzacepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;

5. ndipo ulemerero wa Yehova udzabvumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena comweco,

6. Mau a wina ati, Pfuula. Ndipo ndinati, Kodi ndipfuule ciani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;

7. udzu unyala, duwa lifota; cifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.

8. Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zacikhalire.

9. Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitari; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena ku midzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!

10. Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wace udzalamulira; taonani, mphoto yace iri ndi Iye, ndipo cobwezera cace ciri patsogolo pa Iye.

11. Iye adzadyetsa zoweta zace ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pacapa pace, nadzawatengera pa cifuwa cace, ndipo adzatsogolera bwino bwino zimene ziyamwitsa.

12. Ndani wayesa madzi m'dzanja lace, nayesa thambo ndi cikhato, ndi kudzaza pfumbi la nthaka m'nsengwa, ndi kuyesa mapiri m'mbale zoyesera, ndi zitunda m'mulingo?

13. Ndani anapangira mzimu wa Yehova, kapena kukhala phungu lace, ndi kumphunzitsa Iye?

14. Iye anakhala upo ndi yani, ndipo ndani analangiza Iye ndi kumphunzitsa m'njira ya ciweruzo, ndi kumphunzitsa nzeru ndi kumuonetsa njira ya luntha?

15. Taonani, amitundu akunga dontho la m'mtsuko, nawerengedwa ngati pfumbi losalala la m'muyeso; taonani atukula zisumbu ngati kanthu kakang'ono.

16. Ndipo Lebano sakwanira kutentha, ngakhale nyama zace sizikwanira nsembe yopsereza.

17. Amitundu onse ali cabe pamaso pa Iye; awayesa ngati cinthu cacabe, ndi copanda pace,

18. Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi cithunzithunzi cotani?

19. Pano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golidi analikuta ndi golidi, naliyengera maunyolo asiliva.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 40