Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 40:17-31 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Amitundu onse ali cabe pamaso pa Iye; awayesa ngati cinthu cacabe, ndi copanda pace,

18. Mudzafanizira Mulungu ndi yani tsopano, kapena kumyerekeza ndi cithunzithunzi cotani?

19. Pano losema mmisiri analisungunula, ndipo wosula golidi analikuta ndi golidi, naliyengera maunyolo asiliva.

20. Wosowa nsembe yoteroyo asankha mtengo umene sungabvunde, iye adzisankhira yekha munthu mmisiri waluso, akonze fano losema, limene silisunthika.

21. Kodi inu simunadziwe? kodi inu simunamve? kodi sanakuuzani inu ciyambire? kodi inu simunadziwitse ciyambire mayambiro a dziko lapansi?

22. Ndi Iye amene akhala pamwamba pa malekerezo a dziko lapansi, ndipo okhalamo akunga ziwala; amene afutukula thambo ngati cinsaru, naliyala monga hema wakukhalamo;

23. amene asandutsa akalonga kuti akhale acabe, nasandutsa oweruza a dziko lapansi akhale opanda pace,

24. Inde sanaokedwe, inde sanafesedwe; inde, muzu wao sunazike pansi; koma Iye anawaombetsera mphepo, ndipo afota, ndipo kabvumvulu awacotsa monga ciputu.

25. Mudzandifanizira Ine ndi yani tsono, kuti ndilingane naye, ati Woyerayo.

26. Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene aturutsa khamu lao ndi kuziwerenga; azicha zonse maina ao, ndi mphamvu zace zazikuru, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.

27. Bwanji iwe, Yakobo, umati, ndi bwanji umanena iwe, Israyeli, Njira yanga yabisika kwa Yehova; ndipo ciweruzo ca Mulungu wanga candipitirira?

28. Kodi iwe sunadziwe? kodi sunamve? Mulungu wacikhalire, Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi, salefuka konse, salema; nzeru zace sizisanthulika.

29. Iye alimbitsa olefuka, naonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu.

30. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu:

31. koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga kuma osalema; adzayenda koma osalefuka.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 40