Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 4:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo akazi asanu ndi awiri adzagwira mwamuna mmodzi tsiku limenelo, nati, Ife tidzadya cakudya cathu cathu ndi kubvala zobvala zathu zathu; koma tichedwe dzina lako; cotsa citonzo cathu.

2. Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, cipatso ca nthaka cidzakhala cokometsetsa ndi cokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israyeli.

3. Ndipo padzakhala, kuti iye amene asiyidwa m'Ziyoni, ndi iye amene atsala m'Yerusalemu, adzachedwa woyera; ngakhale yense amene walembedwa mwa amoyo m'Yerusalemu;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 4