Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 34:8-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pakuti liri tsiku la kubwezera la Yehova, caka cakubwezera cilango, mlandu wa Ziyoni.

9. Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi pfumbilo lidzasanduka suifure, ndi dziko lacelo lidzasanduka matope oyaka moto.

10. Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wace udzakwera nthawi zonse; m'mibadwo mibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.

11. Koma bvuo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo cingwe coongolera ca cisokonezo, ndi cingwe colungamitsa ciriri cosatha kucita kanthu.

12. Iwo adzaitana mfulu zace zilowe m'ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ace onse adzakhala cabe.

13. Ndipo minga idzamera m'nyumba zace zazikuru, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwace; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.

14. Ndipo zirombo za m'cipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzace; inde mancici adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.

15. Kumeneko njoka yotumpha idzapanga cisanja cace, niikira, niumatira, niswa mumthunzi mwace; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzace.

16. Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wace wasonkhanitsa iwo.

17. Ndipo Iye wacita maere, cifukwa ca zirombozi, ndipo dzanja lace lazigawira dzikolo ndi cingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwo mibadwo, zidzakhala m'menemo.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 34