Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 34:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko limve, ndi za mommo; dziko ndi zinthu zonse zoturukamo.

2. Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nacitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa,

3. Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.

4. Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.

5. Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.

6. Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa ana a nkhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a imso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m'Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.

7. Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko lao lidzakhuta ndi mwazi, ndi pfumbi lao lidzanona ndi mafuta.

8. Pakuti liri tsiku la kubwezera la Yehova, caka cakubwezera cilango, mlandu wa Ziyoni.

9. Ndipo mitsinjeyo idzasanduka matope akuda, ndi pfumbilo lidzasanduka suifure, ndi dziko lacelo lidzasanduka matope oyaka moto.

10. Sadzazimikai usiku, ngakhale usana; utsi wace udzakwera nthawi zonse; m'mibadwo mibadwo lidzakhala labwinja, palibe amene adzapitapo nthawi za nthawi.

11. Koma bvuo ndi nungu zidzakhalamo, ndipo kadzidzi ndi khungubwi adzakhala m'menemo, ndipo Mulungu adzatambalika pamenepo cingwe coongolera ca cisokonezo, ndi cingwe colungamitsa ciriri cosatha kucita kanthu.

12. Iwo adzaitana mfulu zace zilowe m'ufumu, koma sizidzaonekako; ndi akalonga ace onse adzakhala cabe.

13. Ndipo minga idzamera m'nyumba zace zazikuru, khwisa ndi mitungwi m'malinga mwace; ndipo adzakhala malo a ankhandwe, ndi bwalo la nthiwatiwa.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 34