Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 33:14-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Ocimwa a m'Ziyoni ali ndi mantha, kunthunthumira kwadzidzimutsa anthu opanda Mulungu. Ndani mwa ife adzakhala ndi moto Wakunyeketsa? ndani mwa ife adzakhala ndi zotentha zacikhalire?

15. Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ace kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ace kusamva za mwazi, natsinzina maso ace kusayang'ana coipa;

16. iye adzakhala pamsanje; malo ace ocinjikiza adzakhala malinga amiyala; cakudya cace cidzapatsidwa kwa iye; madzi ace adzakhala cikhalire.

17. Maso ako adzaona mfumu m'kukongola kwace; iwo adzaona dziko lakutari.

18. Mtima wako udzaganizira zoopsya; mlembi ali kuti? ali kuti iye amene anayesa msonkho? ali kuti iye amene anawerenga nsanja?

19. Iwe sudzaona anthu aukali, anthu a mau anthulu, amene iwe sungazindikire; a lilume lacibwibwi, limene iwe sungalimve.

20. Tayang'ana pa Ziyoni, mudzi wa mapwando athu; maso ako adzaona Yerusalemu malo a phe, cihema cimene sicidzasunthidwa, ziciri zace sizidzazulidwa konse, zingwe zace sizidzadulidwa.

21. Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife m'cifumu, malo a nyanja zacitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikuru sizidzapita pamenepo.

22. Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.

23. Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wace, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo colanda cacikulu, cofunkha cinagawanidwa; wopunduka nafumfula.

24. Ndipo wokhalamo sadzanena, Ine ndidwala; anthu okhala m'menemo, adzakhululukidwa mphulupulu zao.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 33