Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 30:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka okhulupirira Aigupto. Tsoka kwa ana opanduka, ati Yehova, amene atenga uphungu koma si pa Ine; napangana pangano opanda mzimu wanga, kuti aonjezere cimo ndi cimo;

2. amene ayenda kutsikira ku Aigupto, osafunsa kukamwa kwanga, kudzilimbitsa iwo okha ndi li mphamvu za Farao, ndi kukhulupirira mthunzi wa Aigupto

3. Cifukwa cace mphamvu za Farao zidzakhala kwa inu manyazi, ndi kukhulupirira mthunzi wa Aigupto kudzakhala cisokonezo canu.

4. Pakuti akalonga ace ali pa Zaani, ndi mithenga yace yafika ku Hanesi.

5. Iwo onse adzakhala ndi manyazi, ndi anthu amene sangapindule nao kanthu, amene sakhala kwa iwo thangata, pena phindu, koma manyazi ndi citonzo.

6. Katundu wa zirombo za kumwera.M'dziko lobvuta ndi lopweteka, kumeneko kucokera mkango waukazi, ndi wamphongo, mphiri, ndi njoka youluka yamoto, iwo anyamula cuma cao pamsana pa aburu, ndi ang'ono zolemera zao pa malinundu a ngamila, kunka kwa anthu amene sadzapindula nao.

7. Pakuti thangata la Aigupto liri lacabe, lopanda pace; cifukwa cace ndamucha wonyada, wokhala cabe.

8. Tsopano pita, ukalembe mauwa pamaso pao pathabwa, nuwalembe m'buku, kuti akakhalebe ku nthawi yam'tsogolo, mboni ya masiku onse.

9. Pakuti ali anthu opanduka, ana onama, ana osafuna kumva cilamulo ca Yehova;

10. amene amati kwa alauli, Mtima wanu usapenye; ndi kwa aneneri, Musanenere kwa ife zinthu zoona, munene kwa ife zinthu zamyadi, munenere zonyenga;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 30