Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 3:7-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. tsiku limenelo adzakweza mau ace, kuti, Sindine wociritsa, cifukwa kuti m'nyumba mwanga mulibe cakudya kapena cobvala; inu simudzandiyesa ine wolamulira anthu.

8. Cifukwa kuti Yerusalemu wapasulidwa, ndi Yuda wagwa; cifukwa kuti lilume lao ndi macitidwe ao akana Yehova, kuti autse mkwiyo wa m'maso a ulemerero wace.

9. Maonekedwe a nkhope zao awacitira iwo mboni; ndipo amaonetsa ucimo wao monga Sodomu, saubisa. Tsoka kwa moyo wao! cifukwa iwo anadzicitira zoipa iwo okha.

10. Nenani za wolungama, kuti kudzamkomera iye; cifukwa oterowo adzadya zipatso za macitidwe ao.

11. Tsoka kwa woipa! kudzamuipira; cifukwa kuti mphotho ya manja ace idzapatsidwa kwa iye.

12. Anthu anga awabvuta ndi ana, awalamulira ndi akazi. Anthu anga inu, iwo amene akutsogolerani, ndiwo akucimwitsani, naononga njira zanu zoyendamo.

13. Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.

14. Yehova adzalowa monenera mirandu ndi okalamba a anthu ace, ndi akuru ace: Ndinu amene mwadya munda wamphesa, zofunkha za waumphawi ziri m'nyumba zanu;

15. muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? ati Ambuye Yehova wa makamu.

16. Komanso Yehova ati, Cifukwa kuti ana akazi a Ziyoni angodzikuza atakweza makosi ao, ndi maso ao adama nayenda nanyang'ama poyenda pao naliza zigwinjiri za mapazi ao;

17. cifukwa cace Ambuye adzacita nkanambo pa liwombo la ana akazi a Ziyoni, ndipo Yehova adzabvundukula m'cuuno mwao.

18. Tsiku limenelo Ambuye adzacotsa zigwinjiri zao zokoma, ndi zitunga, ndi mphande;

19. mbera, ndi makoza, ndi nsaru za pankhope;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 3