18. Ndipo tsiku limenelo gonthi adzam va mau a m'buku, ndi maso akhungu adzaona poturuka m'zoziya ndi mumdima.
19. Ofatsanso kukondwa kwao kudzacuruka mwa Yehova, ndi aumphawi a mwa anthu adzakondwerera mwa Woyera wa Israyeli.
20. Pakuti woopsya wagoma, ndi wonyoza watha, ndi onse odikira zolakwa alikhidwa;
21. amene apalamulitsa munthu mlandu, namchera msampha iye amene adzudzula pacipata, nambweza wolungama ndi cinthu cacabe.
22. Cifukwa cace Yehova amene anaombola Abrahamu, atero za banja la Yakobo: Yakobo sadzakhala ndi manyazi tsopano, ngakhale nkhope yace tsopano sidzagwa.
23. Koma pamene iye aona ana ace, nchito ya manja anga, pakati pa iye, iwo adzayeretsa dzina langa; inde, iwo adzayeretsa Woyera wa Yakobo, nadzaopa Mulungu wa Israyeli.