Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 29:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Eya Arieli, Arieli, mudzi umene Davide anamangapo zithando! oniezerani caka ndi caka; maphwando afikenso;

2. pamenepo ndidzasautsa Arieli, ndipo padzakhala maliro ndi kulira; koma iye adzakhala kwa Ine monga Arieli.

3. Ndipo ndidzamanga zithando kuzungulira iwe ponse, ndipo ndidzamanga linga ndi kuunjika miulu yakumenyanirana ndi iwe.

4. Ndipo iwe udzagwetsedwa pansi, nudzanena uli pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala pansi koturuka m'pfumbi; ndi mau ako adzakhala ngati a wina amene ali ndi mzimu wobwebweta, kucokera pansi, ndi kulankhula kwako kudzakhala konong'ona kocokera m'pfumbi,

5. Koma khamu la acilendo ako lidzafanana ndi pfumbi losalala, ndi khamu la oopsya lidzakhala monga mungu wocokacoka; inde kudzaoneka modzidzimuka dzidzidzi.

6. Ndipo Yehova wa makamu adzamzonda ndi bingu, ndi cibvomezi, ndi mkokomo waukuru, kabvumvulu, ndi mkuntho, ndi lawi la moto wonyambita.

7. Ndipo khamu la mitundu yonse yomenyana ndi Arieli, ngakhale yonse yomenyana naye ndi linga lace, ndi kumsautsa idzafanana ndi loto, masomphenya a usiku.

8. Ndipo kudzafanana ndi munthu wanjala, pamene alota, ndipo, taonani, akudya; koma auka, ndipo m'kati mwace muli zi; kapena monga munthu waludzu pamene alota, ndipo, taonani, akumwa; koma auka ndipo taonani walefuka, ndipo m'kati mwace muli gwa; momwemo lidzakhala khamu la mitundu yonse yomenyana ndi phiri la Ziyoni.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 29