9. Ndi moyo wanga ndinakhumba Inu usiku; inde ndi mzimu wanga wa mwa ine ndidzafuna Inu mwakhama; pakuti pamene maweruziro anu ali pa dziko lapansi, okhala m'dziko lapansi adzaphunzira cilungamo.
10. Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira cilungamo; m'dziko la macitidwe oongoka, iye adzangocimwa, sadzaona cifumu ca Yehova.
11. Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona cangu canu ca kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamariza adani anu.
12. Yehova, udzatikhazikitsira mtendere; pakuti mwatigwirira nchito zathu zonse.
13. Yehova Mulungu wathu, pamodzi ndi Inu ambuye ena adatilamulira ife; koma mwa Inu nokha tidzachula dzina lanu.
14. Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; cifukwa cace Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa cikumbukiro cao conse.
15. Mwacurukitsa mtundu, Yehova, mwacurukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.
16. Yehova, iwo adza kwa Inu mobvutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.
17. Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.
18. Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.