Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 26:14-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Iwo afa, atha, sadzakhalanso ndi moyo; ali mizimu, sadzauka; cifukwa cace Inu munawazonda, ndi kuwaononga, mwathetsa cikumbukiro cao conse.

15. Mwacurukitsa mtundu, Yehova, mwacurukitsa mtundu; Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.

16. Yehova, iwo adza kwa Inu mobvutika, iwo anathira pemphero, muja munalikuwalanga.

17. Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yace yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kupfuula m'zowawa zace; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.

18. Ife tinali ndi pakati, ife tinamva zopweteka, tafanana ngati tabala mphepo; sitinacite cipulumutso ciri conse pa dziko lapansi; ngakhale okhala m'dziko lapansi sanagwe.

19. Akufa anu adzakhala ndi moyo; mitembo yao idzauka. Ukani muyimbe, inu amene mukhala m'pfumbi; cifukwa mame ako akunga mame a pamasamba, ndipo dziko lapansi lidzaturutsa mizimu.

20. Idzani, anthu anga, lowani m'zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthawi kufikira mkwiyo utapita.

21. Pakuti taonani, Yehova adza kucokera ku malo ace kudzazonda okhala pa dziko lapansi, cifukwa ca kuipa kwao; dziko lidzabvumbulutsa mwazi wace, ndipo silidzabvundikiranso ophedwa ace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 26