Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 24:9-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Iwo sadzamwa vinyo ndi kuyimba nyimbo; cakumwa caukali cidzawawa kwa iwo amene acimwa.

10. Mudzi wosokonezeka wagwetsedwa pansi; nyumba zonse zatsekedwa, kuti asalowemo munthu.

11. Muli mpfuu m'makwalala cifukwa ca vinyo; kukondwa konse kwadetsedwa, kusangalala kwa dziko kwatha.

12. M'mudzi mwatsala bwinja, ndi cipata camenyedwa ndi cipasuko.

13. Cifukwa cace padzakhala cotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo waazitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ace.

14. Amenewa adzakweza mau ao, nadzapfuula; cifukwa ca cifumu ca Yehova, iwo adzapfuula zolimba panyanja.

15. Cifukwa cace lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israyeli, m'zisumbu za m'nyanja.

16. Kucokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa ine! amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.

17. Mantha ndi dzenje ndi msampha ziri pa iwe, wokhala m'dziko.

18. Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsya, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.

19. Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi liri kugwedezeka kopambana.

20. Dziko lapansi lidzacita dzandi dzandi, ngati munthu woledzera, ndi kunjenjemera, ngati cilindo; ndi kulakwa kwace kudzalilemera, ndipo lidzagwa losaukanso.

21. Ndipo padzali tsiku limenelo, kuti Yehova adzazonda kumwamba khamu la kumwamba, ndi mafumu a dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 24