Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 22:16-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ucitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.

17. Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba.

18. Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dzido lalikuru; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magareta a ulemerero wako, iwe wocititsa manyazi banja la mbuye wako.

19. Ndipo Ine ndidzakuturutsa iwe mu nchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako.

20. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ine ndidzaitana mtumiki wanga, Eliakimu mwana wa Hilikiya:

21. ndipo ndidzambveka iye cobvala cako, ndi kumlimbikitsa ndi lamba lako, ndipo ndidzapereka ulamuliro wako m'dzanja lace; ndipo iye adzakhala atate wa okhala m'Yerusalemu ndi a nyumba ya Yuda.

22. Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pace, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.

23. Ndipo ndidzamkhomera iye ngati msomali polimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wace.

24. Ndipo iwo adzapacika pa iye ulemerero wonse wa banja la atate wace, obadwa ndi ana, mbiya zonse zazing'ono, ngakhale zikho ndi aguda omwe.

25. Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, msomali wokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopacikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 22