Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 22:13-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.

14. Ndipo Yehova wa makamu wadzibvumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu coipa cimeneci sicidzacotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.

15. Atero Ambuye Yehova wa makamu, Muka, pita iwe kwa kapitao uyu, kwa Sebina woyang'anira nyumba, ndi kuti,

16. Ucitanji iwe kuno, ndimo ndani ali nawe kuno, kuti iwe wagoba manda kuno, ndi kudzigobera manda pamwamba, ndi kudzisemera mogonamo m'thanthwe.

17. Taona Yehova adzakuponya iwe zolimba, monga mwamuna wamphamvu, inde adzakufumbata zolimba.

18. Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dzido lalikuru; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magareta a ulemerero wako, iwe wocititsa manyazi banja la mbuye wako.

19. Ndipo Ine ndidzakuturutsa iwe mu nchito yako, ndi kukutsitsa iwe pokhala pako.

20. Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ine ndidzaitana mtumiki wanga, Eliakimu mwana wa Hilikiya:

21. ndipo ndidzambveka iye cobvala cako, ndi kumlimbikitsa ndi lamba lako, ndipo ndidzapereka ulamuliro wako m'dzanja lace; ndipo iye adzakhala atate wa okhala m'Yerusalemu ndi a nyumba ya Yuda.

22. Ndipo ndidzaika mfungulo wa nyumba ya Davide paphewa pace, ndipo iye adzatsegula, ndipo palibe wina adzatseka, iye adzatseka ndipo palibe wina adzatsegula.

23. Ndipo ndidzamkhomera iye ngati msomali polimba; ndipo iye adzakhala mpando wa ulemerero wa banja la atate wace.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 22