Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 21:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Katundu wa cipululu ca kunyanja. Monga akabvumvulu a kumwela apitirira, kufumira kucipululu ku dziko loopsya.

2. Masomphenya obvuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Media iwe; kuusa moyo kwace konse ndakutonthoza.

3. Cifukwa cace m'cuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndicita mantha sindingathe kuona.

4. Mtima wanga uguguda, mantha andiopsetsa ine; cizitezite cimene ndinacikhumba candisandukira kunthunthumira.

5. Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta cikopa.

6. Pakuti Ambuye atero kwa ine, Muka, ika mlonda anene cimene aciona;

7. ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiri awiri, khamu la aburu, khamu la ngamila, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.

8. Ndipo iye anapfuulitsa ngati mkango, Ambuye inu, ine ndiimabe pamwamba pa nsanja nthawi ya usana, ndipo ndiikidwa mu ulonda wanga usiku wonse;

9. ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apaakavalo awiri awiri. Ndipo iye anayankha nati, Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yace asweka, nagwa pansi.

Werengani mutu wathunthu Yesaya 21