Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Yesaya 20:1-3 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Caka cimene kazembe wa ku Asuri anafika ku Asidodi, muja Sarigoni mfumu ya Asuri anamtumiza iye, ndipo iye anamenyana ndi Asidodi, naugonjetsa.

2. Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule ciguduli m'cuuno mwako, nucicotse, nubvule nsapato yako ku phazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda marisece, ndi wopanda nsapato,

3. Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda marisece ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale cizindikilo ndi codabwitsa kwa Aigupto ndi kwa Etiopia;

Werengani mutu wathunthu Yesaya 20